Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 35:11-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. kacisi, hema wace, ndi cophimba cace, zokowera zace, ndi matabwa ace, mitanda yace, mizati, nsanamira, ndi nsici zace, ndi makamwa ao;

12. likasa, ndi mphiko zace, cotetezerapo, ndi nsaru yocinga yotseka;

13. gome, ndi mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, ndi mkate woonekera;

14. ndi coikapo nyali ca kuunika, ndi zipangizo zace, ndi nyali zace, ndi mafuta a kuunika;

15. ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zace, ndi mafuta odzoza, ndi cofukiza ca pfungo lokoma, ndi nsaru yotsekera pakhomo, pa khomo la kacisi;

16. guwa la nsembe yopereza, ndi made amkuwa, mphiko zace, ndi zipangizo zace zonse, mkhate ndi tsinde lace;

17. nsaru zocingira za kubwalo, nsici zace, ndi makamwa ace, ndi nsaru yotsekera ku cipata ca pabwalo;

18. ziciri za cihema, ndi ziciri za kubwalo, ndi zingwe zao;

19. zobvala za kutumikira nazo m'maopatulika, zobvala zopatulika za. Aroni wansembe, ndi zobvala za ana ace, zakugwira nazo nchito ya nsembe.

20. Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka pamaso pa Mose.

21. Ndipo anadza, ali yense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wace wamfunitsa, nabwera naco copereka ca Yehova, ca ku nchito ya cihema cokomanako, ndi ku utumiki wace wonse, ndi ku zobvala zopatulika.

22. Ndipo anadza amuna ndi akazi, onse akufuna mtima eni ace, nabwera nazo mphete za mphuno, mphete za m'makutu, ndi mphete zosindikizira, ndi zidzingwiri, zonsezi zokometsera zagolidi; inde yense wakupereka kwa Yehova copereka cagolidi.

23. Ndipo ali yense kwao kunapezeka lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi, ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo.

24. Yense wakupereka copereka ca siliva ndi mkuwa, anabwera naco copereka ca Yehova; ndi yense amene kwao kunapezeka mtengo wasitimu wa ku macitidwe onse a nchitoyi, anabwera nao.

25. Ndi akazi onse a mtima waluso anapota ndi manja ao, nabwera nalo thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

26. Ndi akazi onse ofulumidwa mtima ndi luso anapota ubweyawo wa mbuzi.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 35