Ndipo anadza, ali yense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wace wamfunitsa, nabwera naco copereka ca Yehova, ca ku nchito ya cihema cokomanako, ndi ku utumiki wace wonse, ndi ku zobvala zopatulika.