Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 33:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga,

13. Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.

14. Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.

15. Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kucokera kuno.

16. Pakuti cidziwfka ndi ciani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?

17. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ici comwe wanenaci ndidzacita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako.

18. Ndipo anati, Ndionetsenitu ulemerero wanu.

19. Ndipo iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzachula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzacitira ufulu amene ndidzamcitira ufulu; ndi kucitira cifundo amene ndidzamcitira cifundo.

20. Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.

21. Ndipo Yehova anati, Taona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe;

22. ndipo kudzakhala, pakupitira olemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitira;

23. ndipo pamene ndicotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 33