Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 32:5-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuciona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pace; ndipo Aroni anapfuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.

6. Ndipo m'mawa mwace anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.

7. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kucokera m'dziko la Aigupto wadziipsa;

8. wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwana wa ng'ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israyeli, imene inakukweza kucokera m'dziko la Aigupto,

9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;

10. ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukuru.

11. Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawaturutsa m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lolimba?

12. Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.

13. Kumbukilani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzichula nokha, amene munanena nao, Ndidzacurukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale colowa cao nthawi zonse.

14. Ndipo Yehova analeka coipa adanenaci, kuwacitira anthu ace.

15. Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lace; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali yina ndi inzace yomwe.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 32