Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 32:10-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukuru.

11. Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawaturutsa m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lolimba?

12. Akaneneranji Aaigupto; ndi kuti, Anawaturutsa coipa, kuti awaphe m'mapiri, ndi kuwatha pankhope pa dziko lapansi? Pepani, lekani coipaco ca pa anthu anu.

13. Kumbukilani Abrahamu, Isake ndi Israyeli, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzichula nokha, amene munanena nao, Ndidzacurukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale colowa cao nthawi zonse.

14. Ndipo Yehova analeka coipa adanenaci, kuwacitira anthu ace.

15. Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lace; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali yina ndi inzace yomwe.

16. Ndipo magomewo ndiwo nchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.

17. Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kupfuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kucigono.

18. Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kupfuula kwa olakika, kapena la kupfuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe.

19. Ndipo kunali, pamene anayandikiza cigono, anaona mwana wa ng'ombeyo ndi kubvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwace, nawaswa m'tsinde mwa phiri.

20. Ndipo anatenga mwana wa ng'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israyeli.

21. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakucitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukuru kotere?

22. Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba coipa.

23. Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kucokera m'dziko la Aigupto, sitidziwa comwe camgwera.

24. Ndipo ndinanena nao, Ali yense ali naye golidi amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinaciponya m'moto, ndimo anaturukamo mwana wa ng'ombe uyu.

25. Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 32