Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 3:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndipo ndatsikira kuwalanditsa m'manja a anthu a Aigupto, ndi kuwatumtsa m'dziko lila akwere nalowe m'dziko labwino ndi lalikuru, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi; ku malo a Akanani, ndi Ahiti ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi.

9. Ndipo tsopano, taona kulira kwa ana a Israyeli kwandifikira; ndapenyanso kupsinjika kumene Aaigupto awapsinja nako.

10. Tiye tsopano, ndikutuma kwa Farao, kuti uturutse anthu anga, ana a Israyeli m'Aigupto.

11. Koma Mose anati kwa Mulungu, Ndine yani ine kuti ndipite kwa Farao, ndi kuti nditurutse ana a Israyeli m'Aigupto?

12. Ndipo iye anati, Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ici ndi cizindikilo ca iwe, cakuti ndakutuma ndine; utaturutsa anthuwo m'Aigupto mudzatumikira Mulungu paphiri pano.

13. Ndipo Mose anati kwa Mulungu, Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nao, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lace ndani? ndikanena nao ciani?

14. Ndipo Molungu anati kwa Mose, INE NDINE YEMWE NDIRI INE. Anatinso, Ukatero ndi ana a Israyeli, INE NDINE wandituma kwa inu.

15. Ndipo Mulungu ananenanso kwa Mose, Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Molungu wa makolo anu, Molungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Molungu wa Yakobo anandituma kwa inu; ili nw dzina langa nthawi yosatha, ici ndi cikumbukiro canga m'mibadwo mibadwo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 3