Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 29:22-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Utengenso mafuta a nkhosa yamphongoyo, ndi me ira, ndi mafuta akukuta mat umbo, ndi cokuta ca mphafa, ndi imso ziwiri, ndi mafuta ali pamenepo, ndi mwendo wam'mwamba wa ku dzanja lamanja; pakuti ndiyo nkhosa yamphongo ya kudzaza manja;

23. ndi mkate wamphumphu umodzi, ndi kamtanda ka mkate wosanganiza ndi mafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, ziri mu mtanga wa mkate wopanda cotupitsa wokhala pamaso pa Yehova;

24. ndipo uike zonsezo m'manja a Aroni, ndi m'manja a ana ace amuna; nuziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

25. Pamenepo uzilandire m'manja mwao, ndi kuzipsereza pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, zicite pfungo lokoma pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

26. Ndipo utenge nganga ya nkhosa yamphongo yodzaza manja ya Aroni, ndi kuiweyula ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo ikhale gawo lako.

27. Ndipo upatule nganga va nsembe yoweyula, ndi mwendo wam'mwamba wa nsembe yokweza, imene anaiweyula, ndi imene anaikweza, za nkhosa yamphongo yakudzaza manja; ziri za Aroni, ndi za ana ace amuna;

28. ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ace amuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israyeli; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israyeli, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.

29. Ndipo zobvala zopatulika za Aroni zikhale za ana ace amuna pambuyo pace, kuti awadzoze atazibvala, nadzaze manja ao atazibvala;

30. mwana wace wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwace azibvala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'cihema cokomanako kutumikira m'malo opatulika.

31. Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nayama yace m'malo opatulika.

32. Ndipo Aroni ndi ana ace amuna adye nyama ya nkhosa yamphongoyo, ndi mkate uli mumtanga, pa khomo la cihema cokomanako.

33. Ndipo adye zimene anacita nazo coteteza, kuti awadzaze manja ndi kuwapatulitsa; koma mlendo asadyeko, pakuti nzopatulika izi.

34. Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza ncopatulika ici.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 29