Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 20:10-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. koma tsiku lacisanu ndi ciwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire nchito iri yonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wanchito wako wamwamuna, kapena wanchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako;

11. cifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamariza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula tsiku ladsanu ndi ciwiri; cifukwa cace Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.

12. Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti acuruke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

13. Usaphe.

14. Usacite cigololo.

15. Usabe.

16. Usamnamizire mnzako.

17. Usasirire nyumba yace ya mnzako, usasirire mkazi wace wa mnzako, kapena wanchito wace wamwamuna, kapena wanchito wace wamkazi, kapena ng'ombe yace, kapena buru wace, kapena kanthu kali konse ka mnzako.

18. Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga, ndi phiri lirikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.

19. Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe,

20. Ndipo Mose anati kwa anthu, Musaope; pakuti Mulungu wadza kukuyesani ndi kuti kumuopa iye kukhale pamaso panu, kuti musacimwe.

21. Ndipo anthu anaima patali, koma Mose anayandikiza ku mdima waukuru kuli Mulungu.

22. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uzitero ndi ana a Israyeli, kuti, Mwapenya nokha kuti ndalankhula nanu, kucokerakumwamba.

23. Musapange milungu yasiliva ikhale pamodzi ndi Ine; musadzipangire milungu yagolidi.

24. Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomweponsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; pali ponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.

25. Ndipo ukandimangira guwa la nsembe lamiyala, usalimanga ndi miyala yosema; ukakwezapo cosemera cako, waliipsa.

26. Kapena usakwere ndi makwerero ku guwa langa la nsembe, kuti angaoneke marisece ako pamenepo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 20