Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 2:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anaturukira kukazonda abale ace, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu M-aigupto ali kukantha Mhebri, wa abale ace.

12. Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha M-aigupto, namfotsera mumcenga.

13. M'mawa mwace anaturukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wocimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?

14. Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkuru ndi woweruza wathu? kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha M-aigupto? Ndipo Mose anacita mantha, nanena, Ndithu cinthuci cadziwika.

15. Pamene Farao anacimva ici, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midyani; nakhala pansi pacitsime.

16. Ndipo wansembe wa Midyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimweco kuti amwetse gulu la atate wao.

17. Pamenepo anadza abusa nawapitikitsa; koma Mose anauka nawathandiza, namwetsa gulu lao.

18. M'mene anafika kwa Rehueli atate wao, iye anati, Mwabwera msanga bwanji lero?

19. Ndipo anati two, Munthu M-aigupto anatilanditsa m'manja a abusa, natitungiranso madzi okwanira, namwetsa gululi.

20. Ndipo anati kwa ana ace akazi, Ali kuti iye? Mwamsiyiranji munthuyo? Kamuitaneni, adzadye cakudya.

21. Ndipo Mose anabvomera kukhala naye munthuyo; ndipo anampatsa Mose mwana wace wamkazi Zipora.

22. Ndipo anaona mwana, ndi Mose anamucha dzina lace Gerisomu; pakuti anati, Ndakhala mlendo m'dziko la eni.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 2