Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 19:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzicenjera musakwere m'phiri, musakhudza cilekezero cace; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;

13. dzanja liri lonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale coweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lace azikwera m'phirimo.

14. Ndipo Mose anatsika m'phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zobvala zao.

15. Ndipo anati kwa anthu, Mukonzekeretu tsiku lacitatu nimusayandikiza mkazi.

16. Ndipo kunali tsiku lacitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.

17. Ndipo Mose anaturutsa anthu kutsasa, kuti akomane ndi Mulungu; ndipo anaima patsinde pa phiri.

18. Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wace unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri,

19. Ndipo pamene liu la lipenga linamveka linakulira-kulira, Mose ananena, ndi Mulungu anamyankha ndi mau.

20. Ndipo Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pace pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri; ndi Mose anakwerapo.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 19