Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 14:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo ana a Israyeli analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

23. Ndipo Aaigupto anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magareta ace, ndi apakavalo ace.

24. Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aaigupto, Baubvuta ulendo wa Aaigupto.

25. Ndipo anagurula njinga za magareta ao, nawayendetsa molemetsa; pamenepo Aaigupto anati, Tithawe pamaso pa Israyeli; pakuti Yehova alikuwagwirira nkhondo pa Aaigupto.

26. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aaigupto, magareta ao, ndi apakavalo ao.

27. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja, ndi nyanja inabwerera m'mayendedwe ace mbanda kuca; ndipo Aaigupto pothawa anakomana nayo; ndipo Yehova anakutumula Aaigupto m'kati mwa nyanja.

28. Popeza madziwo anabwerera, namiza magareta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsala wa iwowa ndi mmodzi yense.

29. Koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja; ndi madziwo anakhala ngati khoma kwa iwo, palamanja ndi palamanzere.

30. Comweco Yehova anapulumutsa Israyeli tsiku lomwelo m'manja a Aaigupto; ndipo Israyeli anaona Aaigupto akufa m'mphepete mwa nyanja.

31. Ndipo Israyeli anaiona nchito yaikuru imene Yehova anacitira Aaigupto, ndipo anthuwo anaopa Yehova; nakhulupirira Yehova ndi mtumiki wace Mose.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 14