Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 14:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Si awa maowo tinalankhula nanu m'Aigupto ndi kuti, Tliekeni, kuti tigwirire nchito Aaigupto? pakuti kutumikira Aaigupto kutikomera si kufa m'cipululu ai.

13. Ndipo Mose ananena ndi anthu, Musaope, cirimikani, ndipo penyani cipulumutso ca Yehova, cimene adzakucitirani lero; pakuti Aaigupto mwawaona lerowa simudzawaonansokonse.

14. Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala cere.

15. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Upfuuliranji kwa Ine? lankhula ndi ana a Israyeli kuti aziyenda.

16. Ndipo iwe nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigawe, kuti ana a Israyeli alowe pakati pa nyanja pouma.

17. Ndipo Ine, taonani, ndilimbitsa mitima ya Aaigupto, kuti alowemo powatsata; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao, ndi pa nkhondo yace yonse, pa magareta ace, ndi pa okwera pa akavalo ace.

18. Ndipo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magareta ace, ndi pa okwera pa akavalo ace.

19. Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israyeli, unacokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unacoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;

20. nulowa pakati pa ulendo wa Aaigupto ndi ulendo wa Aisrayeli ndipo mtambo unacita mdima, komanso unaunikira usiku; ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzace usiku wonse.

21. Ndipo Mose anatambasulira dzanja lace kunyanja; ndipo Yehova anabweza nyanja ndi mphepo yolimba ya kum'mawa usiku wonse, naumitsa nyanja; ndipo madziwo anagawikana.

22. Ndipo ana a Israyeli analowa pakati pa nyanja pouma; ndi madziwo anakhala kwa iwo ngati khoma palamanja, ndi palamanzere.

23. Ndipo Aaigupto anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magareta ace, ndi apakavalo ace.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 14