Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Lankhula ndi anthu a Israyeli kuti abwerere m'mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja yamcere, patsogolo pa Baala-Zefoni; pandunji pace mugone panyanja.

3. Ndipo Farao adzanena za ana a Israyeli, Azimidwa dziko, cipululu cawatsekera.

4. Ndipo ndidzalimbitsa mtima wace wa Farao kuti awalondole; ndipo ndidzalemekezedwa pa Farao ndi pa nkhondo yace yonse; pamenepo Aaigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, Ndipo anacita comweco.

5. Ndipo anauza mfumu ya Aigupto kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ace inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ici nciani tacita, kuti talola Israyeli amuke osatigwiriranso nchito?

6. Ndipo anamanga gareta lace, napita nao anthu ace;

7. napita nao magareta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magareta onse a m'Aigupto, ndi akapitao ao onse.

8. Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aigupto, ndipo iye analondola ana a Israyeli; koma ana a Israyeli adaturuka ndi dzanja lokwezeka.

9. Ndipo Aaigupto anawalondola, ndiwo akavalo ndi magareta onse a Farao, ndi apakavalo ace, ndi nkhondo yace, nawapeza ali kucigono kunyanja, pa Pihahiroti, patsogolo pa Baala-Zefoni.

10. Ndipo pamene Farao anayandikira ana a Israyeli anatukula maso ao, taonani, Aaigupto alinkutsata pambuyo pao; ndipo anaopa kwambiri; ndi ana a Israyeli anapfuulira kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 14