Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 12:2-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa caka.

3. Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israyeli ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwana wa nkhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwana wa nkhosa pabanja.

4. Banja likaperewera mwana wa nkhosa, munthu ndi mnzace ali pafupi pa nyumba yace atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwana wa nkhosa monga mwa kudya kwao.

5. Mwana wa nkhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa caka cimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

6. Ndipo mukhale naye cisungire kufikira tsiku lakhumi ndi cinai la mwezi womwe; ndipo bungwe lonse la anthu a Israyeli lizimupha madzulo.

7. Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo.

8. Ndipo azidya nyamayo usiku womwewo, yooca pamoto, ndi mkate wopanda cotupitsa; aidye ndi ndiwo zowawa,

9. Musaidya yaiwisi, kapena yophika ndi madzi konse ai, koma yooca pamoto; muti wace ndi miyendo yace ndi matumbo ace.

10. Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mawayo muipsereze ndi moto:

11. Ndipo muziidya cotero: okwinda m'cuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paskha wa Yehova.

12. Pakuti ndidzapita pakati pa dziko la Aigupto usiku womwewo, ndi kukantha ana oyamba onse m'dziko la Aigupto, anthu ndi zoweta; ndipo ndidzacita maweruzo pa milungu yonse ya Aigupto; Ine ndine Yehova.

13. Ndipo mwaziwo udzakhala cizindikilo kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Aigupto,

Werengani mutu wathunthu Eksodo 12