Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 11:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Yehova anawapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto. Munthuyo Mose ndiyenso wamkuru ndithu m'dziko la Aigupto, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

4. Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzaturuka loe kumka pakati pa Aigupto;

5. ndipo ana onse oyamba a m'dziko la Aigupto adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wacifumu wace, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

6. Ndipo kudzakhala kulira kwakukuru m'dziko lonse la Aigupto, kunalibe kunzace kotere, sikudzakhalanso kunzace kotere.

7. Koma palibe garu adzafunyitsira lilime lace ana onse a Israyeli ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aaigupto ndi Aisrayeli.

8. Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Turukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pace ndidzaturuka. Ndipo anaturuka kwa Farao wakupsa mtima.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 11