Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Cozizwitsa cakhumi: Imfa ya ana oyamba kubadwa

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Watsala moo umodzi ndidzamtengera Farao, ndi Aigupto; pambuyo pace adzakulolani mucoke kuno; pamene akulolani kupita, zoonadi adzakuingitsani kuno konse.

2. Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzace, ndi mkazi yense kwa mnzace, zokometsera zasiliva ndi zagolidi.

3. Ndipo Yehova anawapatsa anthu cisomo pamaso pa Aaigupto. Munthuyo Mose ndiyenso wamkuru ndithu m'dziko la Aigupto, pamaso pa anyamata a Farao, ndi pamaso pa anthu.

4. Ndipo Mose anati, Atero Yehova, Monga pakati pa usiku ndidzaturuka loe kumka pakati pa Aigupto;

5. ndipo ana onse oyamba a m'dziko la Aigupto adzafa, kuyambira mwana woyamba wa Farao wokhala pa mpando wacifumu wace, kufikira mwana woyamba wa mdzakazi wokhala pa miyala yopera; ndi ana onse oyamba a zoweta.

6. Ndipo kudzakhala kulira kwakukuru m'dziko lonse la Aigupto, kunalibe kunzace kotere, sikudzakhalanso kunzace kotere.

7. Koma palibe garu adzafunyitsira lilime lace ana onse a Israyeli ngakhale anthu kapena zoweta; kuti mudziwe kuti Yehova asiyanitsa pakati pa Aaigupto ndi Aisrayeli.

8. Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Turukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pace ndidzaturuka. Ndipo anaturuka kwa Farao wakupsa mtima.

9. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Farao sadzamvera inu; kuti zozizwa zanga zicuruke m'dziko la Aigupto.

10. Ndipo Mose ndi Aroni anacita zozizwa izi zonse pamaso pa Farao; koma Yehova analimbitsa mtima wace wa Farao, ndipo sanalola ana a Israyeli aturuke m'dziko lace.