Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Eksodo 10:4-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako;

5. ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero, kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uti wonse wokuphukirani kuthengo;

6. ndipo lidzadzaza m'nyumba zako, ndi m'nyumba za anyamata ako onse, ndi m'nyumba za Aaigupto onse; sanaciona cotere atate ako kapena makolo ako, kuyambira tsiku lija lakukhala iwo pa dziko lapansi kufikira lero lino. Ndipo anatembenuka, naturuka kwa Farao.

7. Ndipo anyamata ace a Farao ananena naye, Ameneyo amaticitira msampha kufikira liti? Lolani anthuwo amuke, akatumikire Yehova Mulungu wao. Kodi simunayambe kudziwa kuti Aigupto laonongeka?

8. Ndipo anawabwereretsa Mose ndi Aroni kwa Farao, nanena nao, Mukani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma amene adzapitawo ndiwo ani?

9. Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akuru athu, ndi ana athu amuna ndi akazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tiri nao madyerero a Yehova.

10. Ndipo ananena nao, Momwemo, Yehova akhale nanu ngati ndilola inu ndi ana ang'ono anu mumuke; cenjerani, pakuti pali coipa pamaso panu,

11. Cotero ai, mukani tsopano, inu amuna akuru, tumikirani Yehova pakuti ici mucifuna. Ndipo anawapitikitsa pamaso pa Farao.

Werengani mutu wathunthu Eksodo 10