Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 8:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Muzisamalira kucita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kucuruka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.

2. Ndipo mukumbukile njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'cipululu zaka izi makumi anai, kuti akucepetseni, kukuyesani, kudziwa cokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ace, kapena iai.

3. Ndipo anakucepetsani, nakumvetsani odala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwa, angakhale makolo anu sanawadziwa; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakuturuka m'kamwa mwa Yehova.

4. Zobvala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai.

5. Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.

6. Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kumuopa.

7. Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe, ndi la maiwe akuturuka m'zigwa, ndi m'mapiri;

8. dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uci;

9. dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yace nja citsulo, ndi m'mapiri ace mukumbe mkuwa.

10. Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu cifukwa ca dziko lokomali anakupatsani.

11. Cenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino;

12. kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;

13. ndipo zitacuruka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 8