Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 7:20-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Komanso Yehova Mulungu wanu adzatumiza mabvu pakati pao, kufikira ataonongeka otsalawo, ndi akubisala pamaso panu.

21. Musamaopa pamaso pao; popeza Yehova Mulungu wanu ali pakati pa inu, Mulungu wamkuru ndi woopsa.

22. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzataya amitundu awa pang'ono pang'ono; simuyenera kuwaononga msanga, kuti zingakucurukireni zirombo.

23. Koma Yehova Mulungu wanu adzawapereka pamaso panu, nadzawapitikitsa ndi kupitikitsa kwakukuru, kufikira ataonongeka.

24. Adzaperekanso mafumu ao m'dzanja mwanu, ndipo muwafafanize maina ao pansi pa thambo; palibe munthu mmodzi adzaima pamaso panu, kufikira mutawaononga,

25. Mafano osema a milungu yao muwateothe ndi moto; musamasirira siliva ndi golidi ziri pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.

26. Musamalowa naco conyansaci m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi naco; muziipidwa naco konse, ndi kunyansidwa naco konse; popeza ndi cinthu coyenera kuonongeka konse.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 7