Musamalowa naco conyansaci m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi naco; muziipidwa naco konse, ndi kunyansidwa naco konse; popeza ndi cinthu coyenera kuonongeka konse.