Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 6:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwacita m'dziko limene muolokerako kulilandira;

2. kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ace onse ndi malamulo ace, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu acuruke.

3. Potero imvani, Israyeli, musamalire kuwacita, kuti cikukomereni ndi kuti mucuruke cicurukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

4. Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;

5. ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.

6. Ndipo mau awa ndikuuzanilero, azikhala pamtima panu;

7. ndipo muziwaphunzitsa mwacangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

8. Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati cizindikilo, ndipo akhale ngati capamphumi pakati pa maso anu.

9. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.

10. Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;

11. ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 6