Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 4:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Cifukwa cace asungeni, aciteni; pakuti ici ndi nzeru zanu ndi cidziwitso canu pamaso pa mitundu ya anthu akumva malemba ndi kuti, Ndithu mtundu waukuru uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.

7. Pakuti dioloketu mtundu waukuru wa anthu ndi uti, wakukhala ndi Mulungu pafupi pao monga amakhala Yehova Mulungu wathu, pamene pali ponse timaitanira iye?

8. Ndipo mtundu waukuru wa anthu ndi uti, wakukhala nao malemba ndi maweruzo olungama, akunga cilamulo ici conse ndiciika pamaso panu lero lino?

9. Cokhaci, dzicenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwacangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisacoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.

10. Tsikuli munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'Horebe muja Yehova anati kwa ine, Ndisonkhanitsire anthu, ndidzawamvetsa mau anga, kuti aphunzire kundiopa Ine masiku ao onse akukhala ndi moyo pa dziko lapansi, ndi kuti aphunzitse ana ao.

11. Ndipo munayandikiza ndi kuima patsinde pa phiri; ndi phizilo linayaka mota kufikira pakati pa thambo; kunali mdima, ndi mtambo, inde mdima bii.

12. Pamenepo Yehova ananena ndi inu ali pakati pa moto; munamva kunena kwa mau, osaona maonekedwe, koma kunenako.

13. Pamenepo anakufotokozerani cipangano cace, cimene anakulamulirani kucicita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 4