Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 33:16-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndi zinthu zofunikatu za dziko lapansi, ndi kudzala kwace,Ndi cibvomerezo ca iye anakhala m'citsambayo;Mdalitso ufike pa mutu wa Yosefe,Ndi pakati pa mutu wace wa iye wokhala padera ndi abale ace.

17. Woyamba kubadwa wa ng'ombe yace, ulemerero ndi wace;Nyanga zace ndizo nyanga zanjati;Adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi.Iwo ndiwo zikwi khumi za Efraimu,Iwo ndiwo zikwi za Manase.

18. Ndi za Zebuloni anati,Kondwera, Zebuloni, ndi kuturukakwako;Ndi Isakara, m'mahema mwako.

19. Adzaitana mitundu ya anthu afike kuphiri;Apo adzaphera nsembe za cilungamo;Popeza adzayamwa zocuruka za m'nyanja,Ndi cuma cobisika mumcenga.

20. Ndi za Gadi anati,Wodala iye amene akuza Gadi;Akhala ngati mkango waukazi,Namwetula dzanja, ndi pakati pa mutu pomwe.

21. Ndipo anadzisankhira gawo loyamba,Popeza kumeneko kudasungika gawo la wolamulira;Ndipo anadza ndi mafumu a anthu,Anacita cilungamo ca Yehova,Ndi maweruzo ace ndi Israyeli.

22. Ndi za Dani anati,Dani ndiye mwana wa mkango,Wakutumpha moturuka m'Basana.

23. Za Nafitali anati,Nafitali, wokhuta nazo zomkondweretsa,Wodzala ndi mdalitso wa Yehova;Landira kumadzulo ndi kumwela.

24. Ndi za Aseri anati,Aseri adalitsidwe mwa anawo;Akhale wobvomerezeka mwa abale ace,Abviike phazi lace m'mafuta.

25. Nsapato zako zikhale za citsulo ndi mkuwa;Ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.

26. Palibe wina ngati Mulungu, Yesuruni iwe,Wakuyenda wokwera pathambo, kukuthandiza,Ndi pa mitambo m'ukulu wace.

27. Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako;Ndi pansipo pali manja osatha.Ndipo aingitsa mdani pamaso pako,Nati, Ononga.

28. Ndipo Israyeli akhala mokhazikika pa yekha;Kasupe wa Yakobo;Akhala m'dziko la tirigu ndi vinyo;Inde thambo lace likukha mame.

29. Wodala iwe, Israyeli;Akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova,Ndiye cikopa ca thandizo lako,Iye amene akhala lupanga la ukulu wako!Ndi adani ako adzakugonjera; Ndipo udzaponda pa misanje yao.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 33