Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 31:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose anamuka nanena mau awa kwa Israyeli wonse,

2. nati nao, Ndine munthu wa zaka zana ndi makumi awiri lero lino; sindikhozanso kuturuka ndi kulowa ndipo Yehova anati kwa ine, Sudzaoloka Yordano uyu.

3. Yehova Mulungu wanu ndiye adzaoloka pamaso panu, iye ndiye adzaononga amitundu awo pamaso panu, ndipo mudzawalandira. Yoswa ndiye adzakutsogolerani pooloka, monga ananena Yehova.

4. Ndipo Yehova adzawacitira monga anacitira Sihoni ndi Ogi, mafumu a Aamori, ndi dziko lao limene analiononga.

5. Yehova akadzawapereka pamaso panu, muziwacitira monga mwa lamulo lonse ndakuuzani.

6. Khalani amphamvu, limbikani mitima, musamacita mantha, kapena kuopsedwa cifukwa ca iwowa; popeza Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena irukusiyani.

7. Ndipo Mose anaitana Yoswa, nati naye pamaso pa Israyeli wonse, Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao anthu awa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo ao kuwapatsa ilo; ndipo iwe udzawalandiritsa ilo.

8. Ndipo Yehova, iye ndiye amene akutsogolera; iye adzakhala ndi iwe, iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamacita mantha, usamatenga nkhawa.

9. Ndipo Mose analembera cilamulo ici, nacipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kwa akuru onse a Israyeli,

10. Ndipo Mose anawauza, ndi kuti, Pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwiri, pa nyengo yoikika ya m'caka cakulekerera, pa madyerero a misasa;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 31