Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 30:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. pamenepo Yehova Mulungu wanu adzaucotsa ukapolo wanu, ndi kukucitirani cifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.

4. Otayika anu akakhala ku malekezero a thambo, Yehova Mulungu wanu adzakumemezani kumeneko, nadzakutenganiko;

5. ndipo Yehova Mulungu wanu adzakulowetsani m'dziko lidakhala lao lao la makolo anu, nilidzakhala lanu lanu; ndipo adzakucitirani zokoma, ndi kukucurukitsani koposa makolo anu.

6. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.

7. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzaika matemberero awa onse pa adani anu, ndi iwo akukwiya ndi inu, amene anakulondolani.

8. Pamenepo mutembenuke ndi kumvera mau a Yehova, ndi kucita malamulo ace onse amene ndikuuzani lero lino.

9. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakucurukitsirani nchito zonse za dzanja lanu, zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za zoweta zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zikukomereni; popeza Yehova Mulungu wanu adzakondweranso kukucitirani zokoma; monga anakondwera ndi makolo anu;

10. ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ace ndi malemba ace olembedwa m'buku la cilamulo ici; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

11. Pakuti lamulo ili ndikuuzani lero lino, silikulakani kulizindikira, kapena silikhala kutali.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 30