Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 3:21-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo ndinauza Yoswa muja, ndi kuti, Maso ako anapenya zonse Yehova Mulungu wanu anawacitira mafumu awa awiri; momwemo Yehova adzacitira maufumu onse kumene muolokerako.

22. Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo.

23. Ndipo ndinapempha cifundo kwa Yehova nthawi yomwe ija, ndi kuti,

24. Ambuye Yehova, mwayamba Inu kuonetsera mtumiki wanu ukulu wanu, ndi dzanja lanu lamphamvu; pakuti Mulungu ndani m'mwamba kapena pa dziko lapansi wakucita monga mwa nchito zanu, ndi monga mwa mphamvu zanu?

25. Ndioloketu, ndilione dziko lokomali liri tsidya la Yordano, mapiri okoma aja, ndi Lebano.

26. Koma Yehova anakwiya ndi ine, cifukwa ca inu, sanandimvera ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Cikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za cinthuci.

27. Kwera kumwamba ku Pisiga, nukweze maso ako kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwela, ndi kum'mawa, nuyang'ane ndi maso ako; popeza sudzaoloka Yordano uyo.

28. Koma langiza Yoswa, dioloketu numlimbitse mtima, ndi kumkhwimitsa, pakuti adzaoloka pamaso pa anthu awa, nadzawalandiritsa dziko ulionali likhale lao lao.

29. Potero tinakhala m'cigwamo pandunji pa Beti Peori.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 3