Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 25:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.

2. Ndipo kudzali, wocita coipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pace, amwerengere zofikira coipa cace.

3. Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.

4. Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu.

5. Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wafayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wace alowane naye, namtenge akhale mkazi wace, namcitire zoyenera mbale wa mwamuna wace.

6. Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lace la mbale wace wafayo, kuti dzina lace lisafafanizidwe m'Israyeli.

7. Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wace, mkazi wa mbale waceyo azikwera kumka kucipata, kwa akuru, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wace dzina m'Israyeli; safuna kundicitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.

8. Pamenepo akuru a mudzi wace amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;

9. pamenepo mkazi wa mbale wace azimyandikiza pamaso pa akuru, nacotse nsapato yace ku ph zi la mwamunayo, ndi kumthira malobvu pankhope pace, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 25