Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 19:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire midzi itatu.

8. Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;

9. ukadzasunga lamulo ili lonse kulicita, limene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace masiku onse; pamenepo mudzionjezere midzi itatu yina pamodzi ndi itatu iyi;

10. kuti angakhetse mwazi wosacimwa pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu, pangakhale mwazi pa inu.

11. Koma munthu akamuda mnzace, namlalira, ndi kumuukira ndi kumkanth a moyo wace, kuti wafa; nakathawira ku wina wa midzi iyi;

12. pamenepo akuru a mudzi wace atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.

13. Diso lanu lisamcitire cifundo, koma mucotse mwazi wosacimwa m'Israyeli, kuti cikukomereni.

14. Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'colowa canu mudzalandiraci, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 19