Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'colowa canu mudzalandiraci, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.