Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 19:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. pamenepo mudzipatulire midzi itatu pakati pa dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.

3. Mudzikonzere njira, ndi kugawa malire a dziko lanu, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu, patatu; kuti wakupha munthu athawireko.

4. Ndipo mlandu wa munthu wakupha mnzace wakuthawirako nakhala ndi moyo ndiwo: wakupha mnzace osati dala, osamuda kale lonse;

5. monga ngati munthu analowa kunkhalango ndi mnzace kutema mitengo, ndi dzanja lace liyendetsa nkhwangwa kutema mtengo, ndi nkhwangwa iguruka m'mpinimo, nikomana ndi mnzace, nafa nayo; athawire ku wina wa midzi iyi, kuti akhale ndi moyo;

6. kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzace, pokhala mtima wace watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanaparamula imfa, poona sanamuda kale lonse.

7. Cifukwa cace ndikuuzani ndi kuti, Mudzipatulire midzi itatu.

8. Ndipo Yehova Mulungu wanu akakulitsa malire anu, monga analumbirira makolo anu, ndi kukupatsani dziko lonse limene ananena kwa makolo anu kuwapatsa ili;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 19