Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 16:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzicitira Yehova Mulungu wanu Paskha; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakuturutsani m'dziko la Aigupto usiku.

2. Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paskha, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lace.

3. Musamadyera nayo mkaye wa cotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda cotupitsa, ndiwo mkate wa cizunziko popeza munaturuka m'dziko la Aigupto mofulumira; kuti inu kumbukile tsiku loturuka inu m'dziko la Aigupto masiku onse a moyo wanu.

4. Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke cotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa.

5. Simuyenera kuphera nsembe ya Paskha m'midzi yanu iri yonse, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani;

6. koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lace, pamenepo muphere nsembe ya Paskha, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kuturuka inu m'Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 16