Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 15:14-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za padwale, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.

15. Ndipo mukumbukile kuti munali akapolo m'dziko la Aigupto, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; cifukwa cace ndikuuzani ici lero lino.

16. Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituruka kucoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;

17. pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwace, kulikanikiza ndi citseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzicitanso momwemo ndi adzakazi anu.

18. Musamayesa neosautsa, pomlola akucokereni waufulu; popeza anakugwirirani nchito zaka zisanu ndi cimodzi monga wolipidwa wakulandira cowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzicita.

19. Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa nchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.

20. Muzidye caka ndi caka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m'banja mwanu.

21. Koma ikakhala naco cirema, yotsimphina, kapena yakhungu, cirema ciri conse coipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.

22. Muidye m'mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye cimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 15