Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 13:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani cizindikilo kapena cozizwa;

2. ndipo cizindikilo kapena cozizwa adanenaci cifika, ndi kuti, Titsate milungu yina, imene simunaidziwa, ndi kuitumikira;

3. musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.

4. Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ace, ndi kumvera mau ace, ndi kumtumikira iye, ndi kummamatira.

5. Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena cosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, nakuombolani m'nyumba ya akapolo; kuti akuceteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzicotsa coipaco pakati pa inu.

6. Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanu wanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu yina, imene simunaidziwa, inu, kapena makolo anu;

7. ndiyo milungu ya mitundu ya anthu akuzungulira inu, akukhala pafupi pali inu, kapena akukhala patali pali inu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero ena a dziko lapansi;

8. musamabvomerezana naye, kapena kumvera iye; diso lanu lisamcitire cifundo, kapena kumleka, kapena kumbisa;

9. koma muzimupha ndithu; liyambe dzanja lanu kukhala pa iye kumupha, ndi pamenepo dzanja la anthu onse.

10. Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukucetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba va akapolo.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 13