Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 12:28-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Samalirani ndi kumvera mau awa onse ndikuuzaniwa, kuti cikukomereni inu, ndi ana anu akudza m'mbuyo mwanu nthawi zonse, pocita inu zokoma ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29. Pamene Yehova Mulungu wanu akadzadulatu amitundu pamaso panu, kumene mulowako kuwalandira, ndipo mutawalandira, ndi kukhala m'dziko lao,

30. dzicenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? ndicite momwemo inenso.

31. Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti ziri zonse zinyansira Yehova, zimene azida iye, iwowa anazicitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao amuna ndi ana ao akazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.

32. Ciri conse ndikuuzani, mucisamalire kucicita; musamaoniezako, kapena kucepsako.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 12