Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 11:3-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. ndi zizindikilo zace, ndi nchito zace, adazicitira Farao mfumu ya Aigupto, ndi dziko lace lonse pakati pa Aigupto;

4. ndi cocitira iye nkhondo ya Aigupto, akavalo ao, ndi agareta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;

5. ndi cimene anakucitirani m'cipululu, kufikira munadza kumalo kuno;

6. ndi cimene anacitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pace, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israyeli wonse.

7. Koma maso anu anapenya nchito yonse yaikuru ya Yehova anaicita.

8. Potero muzisunga malamulo onsewa ndikuuzani lero lino, kuti mukhale amphamvu, ndi kulowa ndi kulandira dziko, limene mumkako kulilandira;

9. ndi kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, kuti adzawapatsa iwo ndi mbeu zao, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

10. Pakuti dziko limene mumkako kulilandira ndi losanga dziko la Aigupto lija mudaturukako, kumene kuja munafesa mbeu zanu, ndi kuzithirira ndi phazi lanu, monga munda watherere;

11. koma dziko limene mumkako kulilandira ndilo dziko la mapiri ndi zigwa; limamwa madzi a mvula ya kumwamba;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 11