Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 10:1-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Masiku aja Yehova anati kwa ine, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja, nukwere kuno kwa Ine m'phiriumu, nudzipangire likasa lamtengo.

2. Ndipo ndidzalembera pa magomewo mauwo anali pa magome oyamba aja amene unawaswa, ndipo uwaike m'likasamo.

3. Potero ndinapanga likasa la mtengo wasitimu, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga.

4. Ndipo analembera pamagome, monga mwa malembedwe oyamba, mau khumiwo, amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku la kusonkhanako; ndipo Yehova anandipatsa awa.

5. Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi kuika magome m'likasa ndinalipanga, ali m'menemo monga Yehova anandilamulira ine.

6. Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wao kucokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wace anacita nchito ya nsembe m'malo mwace.

7. Kucokerako anamka ulendo ku Gudigoda, ndi kucokera ku Gudigoda kumka ku Yotibata, dziko la mitsinje yamadzi.

8. Masiku aja Yehova anapatula pfuko la Levi, linyamule likasa la cipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kufikira lero lino.

9. Cifukwa cace Levi alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi abale ace; Yehova mwini wace ndiye colowa cace, monga Yehova Mulungu wace ananena naye.

10. Ndipo ndinakhala m'phiri monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku; ndipo Yehova anandimvera ine pameneponso; Yehova sanafuna kukuonongani.

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, tenga ulendo pamaso pa anthu; kuti alowe ndi kulandira dzikoli ndinalumbirira makolo ao kuti ndidzawapatsa.

12. Ndipo tsopano, Israyeli, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanundimtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

13. kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?

14. Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse ziri m'mwemo ndi zace za Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 10