Ndipo ana a Israyeli anayenda ulendo wao kucokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wace anacita nchito ya nsembe m'malo mwace.