Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 9:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Cifukwa cace Yehova wakhala maso pa coipaco, ndi kutifikitsira ico; pakuti Yehova Mulungu wathu ali wolungama mu nchito zace zonse azicita; ndipo sitinamvera mau ace.

15. Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munaturutsa anthu anu m'dziko la Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tacimwa, tacita coipa.

16. Ambuye, monga mwa cilungamo canu conse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zicoke ku mudzi wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zocimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka cotonza ca onse otizungulira.

17. Ndipo tsopano, Mulungu wathu, mumvere pemphero la mtumiki wanu, ndi mapembedzero ace, nimuwalitse nkhope yanu pa malo anu opatulika amene ali opasuka, cifukwa ca Ambuye,

18. Mulungu wanga, cherani khutu, nimumvere, tsegulani maso anu, nimupenye zopasuka zathu, ndi mudzi udachedwawo dzina lanu; pakuti sititula mapembedzero athu pamaso panu, cifukwa ca nchito zathu zolungama, koma cifukwa ca zifundo zanu zocuruka.

19. Ambu ye, imvani; Ambuye, khululukirani; Ambuye, mverani nimucite; musacedwa, cifukwa ca inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anachedwa dzina lanu.

20. Ndipo pakunena ine, ndi kupemphera, ndi kubvomereza cimo langa, ndi cimo la anthu amtundu wanga Israyeli, ndi kutula cipembedzero canga pamaso pa Yehova Mulungu wanga, cifukwa ca phiri lopatulika la Mulungu wanga;

21. inde pakunena ine m'kupemphera, munthu uja Gabrieli, amene ndidamuona m'masomphenya poyamba paja, anauluka mwaliwiro nandikhudza ngati nthawi yakupereka nsembe ya madzulo.

22. Ndipo anandilangiza ine, ndi kulankhula nane, nati, Danieli iwe, ndaturuka tsopano ine kukuzindikiritsa mwaluntha.

23. Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linaturuka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.

24. Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu amtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumariza colakwaco, ndi kutsiriza macimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa cilungamo cosalekeza, ndi kukhomera cizindikilo masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulikitsa.

25. Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kuturuka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi chemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mabvuto.

26. Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mudzi ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwace kudzakhala kwa cigumula, ndi kufikira cimariziro kudzakhala nkhondo; cipasuko calembedweratu.

Werengani mutu wathunthu Danieli 9