9. Ndipo mu imodzi ra izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukuru ndithu, kuloza kumwela, ndi kum'mawa, ndi ku dziko lokometsetsa.
10. Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza.
11. Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimcotsera nsembe yopsereza yacikhalire; ndi pokhala malo ace opatulika panagwetsedwa.
12. Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yacikhalire mwa kulakwa kwace, nigwetsa pansi coonadi, nicita cifuniro cace, nikuzika.