Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 7:11-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pamenepo ndinapenyera cifukwa ca phokoso la mau akuru idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adacipha ciromboci, ndi kuononga mtembo wace, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto.

12. Ndipo zirombo zotsalazo anazicotsera ulamuliro wao, koma anatalikitsa moyo wao, ukhalenso nyengo ndi nthawi.

13. Ndinaona m'masomphenya a usiku, taonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pace.

14. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wace ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wace sudzaonongeka.

15. Koma ine Danieli, mzimu wanga unalaswa m'kati mwa thupi langa, ndi masomphenya a m'mtima mwanga anandibvuta.

16. Ndinayandikira kwa wina wa iwo akuimako ndi kumfunsa za coonadi za ici conse. Ndipo ananena nane, nandidziwitsa kumasulira kwace kwa zinthuzi:

17. Zirombo zazikuru izi zinai ndizo mafumu anai amene adzauka pa dziko lapansi.

18. Koma opatulika la Wam'mwambamwamba adzalandira ufumuwo, ndi kukhala nao ufumu kosatha, ku nthawi zomka muyaya.

19. Pamenepo ndinafuna kudziwa coonadi ca cirombo cacinai cija cidasiyana nazo zonsezi, coopsa copambana, mano ace acitsulo, ndi makadabo ace amkuwa, cimene cidalusa, ndi kuphwanya, ndi kupondereza zotsala ndi mapazi ace;

20. ndi za nyanga khumi zinali pamutu pace, ndi nyanga yina Idaphukayi, imene zidagwa zitatu patsogolo pace; nyangayo idali ndi maso ndi pakamwa pakunena zazikuru, imene maonekedwe ace anaposa zinzace.

21. Ndinapenya, ndipo nyanga yomweyi inacita nkhondo ndi opatulikawo, niwalaka, mpaka inadza Nkhalamba ya kale lomwe;

22. ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo.

23. Anatero, cirombo cacinai ndico ufumu wacinai pa dziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya.

24. Kunena za nyanga khumi, m'ufumu uwu adzauka mafumu khumi, ndi pambuyo pao idzauka yina; iyo idzasiyana ndi oyamba aja, nidzacepetsa mafumu atatu.

25. Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambainwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi cilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lace mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.

26. Koma woweruza mlandu adzakhalako, ndipo adzacotsa ulamuliro wace, kuutha ndi kuuononga kufikira cimariziro.

27. Ndipo ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu a opatulika a Wam'mwambamwamba; ufumu wace ndiwo ufumu wosatha, ndi maiko onse adzamtumikira ndi kummvera.

28. Kutha kwace kwa cinthuci nkuno. Ine Danieli, maganizo anga anandibvuta kwambiri, ndi nkhope yanga inasandulika; koma ndinasunga cinthuci m'mtima mwanga.

Werengani mutu wathunthu Danieli 7