Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 6:16-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Pamenepo inalamula mfumu, ndipo anadza naye Danieli, namponya m'dzenje la mikango. Ndipo mfumu inalankhula, niti kwa Danieli, Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, Iyeyu adzakulanditsa.

17. Ndipo anatenga mwala, nauika pakamwa pa dzenje, niukomera mfumu ndi cosindikizira cace, ndi cosindikizira ca akuru ace, kuti kasasinthike kanthu ka Danieli.

18. Pamenepo mfumu inamuka ku cinyumba cace, nicezera kusala usikuwo, ngakhale zoyimbitsa sanabwera nazo pamaso pace, ndi m'maso mwace munamuumira.

19. Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira ku dzenje la mikango.

20. Ndipo poyandikira padzenje inapfuula ndi mau acisoni mfumu, ninena, niti kwa Danieli, Danieli, mnyamata wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako, amene umtumikira kosalekeza, wakhoza kukulanditsa kwamikango?

21. Pamenepo Danieli anati kwa mfumu, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.

22. Mulungu wanga watuma mthenga wace, natseka pakamwa pa mikango; ndipo siinandipweteka, cifukwa anandiona wosacimwa pamaso pace, pamaso panunso, mfumu, sindinalakwa.

23. Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza aturutse Danieli m'dzenje. Momwemo anamturutsa Danieli m'dzenje, ndi pathupi pace sipadaoneka bala, popeza anakhulupirira Mulungu wace.

24. Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Danieli, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.

25. Pamenepo mfumu Dariyo analembera kwa anthu, mitundu ya anthu, ndi a manenedwe onse okhala pa dziko lonse lapansi, Mtendere ucurukire inu.

26. Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Danieli; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala cikhalire, ndi ufumu wace ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwace kudzakhala mpaka cimariziro.

27. Iye apulumutsa, nalanditsa, nacita zizindikilo ndi zozizwa m'mwamba ndi pa dziko lapansi, ndiye amene anapulumutsa Danieli ku mphamvu ya mikango.

28. Momwemo Danieli amene anakuzikabe pokhala Dariyo mfumu, ndi pokhala mfumu Koresi wa ku Perisiya.

Werengani mutu wathunthu Danieli 6