Ndipo italamulira mfumu, anabwera nao amuna aja adamneneza Danieli, nawaponya m'dzenje la mikango, iwowa, ana ao, ndi akazi ao; ndipo asanafike pansi pa dzenje mikango inawaposa mphamvu, niphwanya mafupa ao onse.