Ndilamulira ine kuti m'maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Danieli; pakuti Iye ndiye Mulungu wamoyo wakukhala cikhalire, ndi ufumu wace ngwosaonongeka, ndi kulamulira kwace kudzakhala mpaka cimariziro.