Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 6:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kudamkomera Dariyo kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu;

2. ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Danieli; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke.

3. Pamenepo Danieli amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.

4. Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola cifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza cifukwa kapena colakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona cosasamala kapena colakwa ciri conse mwa iye.

5. Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola cifukwa ciri conse Danieli amene, tikapanda kumtola ici pa cilamulo ca Mulungu wace.

6. Ndipo akuru awa ndi akalonga anasonkhana kwa mfumu mofulumira, natero nayo, Mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo cikhalire.

7. Akuru onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lacifumu, ndi kuikapo coletsa colimba, kuti ali yense akapempha kanthu kwa mulungu ali yense, kapena kwa munthu ali yense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango,

8. Tsopano, mfumu, mukhazikitse coletsaco, ndi kutsimikiza colembedwaco, kuti cisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.

9. Momwemo mfumu Dariyo anatsimikiza colembedwa ndi coletsaco.

10. Ndipo podziwa Danieli kuti adatsimikiza colembedwaco, analowa m'nyumba mwace, m'cipinda mwace, cimene mazenera ace anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwadamaondo ace tsiku limodzi katatu, napemphera, nabvomereza pamaso pa Mulungu wace monga umo amacitira kale lonse.

11. Pamenepo anasonkhana anthu awa, napeza Danieli alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wace.

Werengani mutu wathunthu Danieli 6