Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 3:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire.

10. Inu mfumu mwalamulira kuti munthu ali yense amene adzamva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, agwadire, nalambire fanolo lagolidi;

11. ndi yense wosagwadira ndi kulambiraadzaponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

12. Alipo Ayuda amene munawaika ayang'anire nchito ya dera la ku Babulo, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, amuna awa, mfumu, sanasamalira inu, satumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.

13. Pamenepo Nebukadinezara, mumkwiyo ndi m'ukali wace, anawauza abwere nao Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Ndipo anabwera nao amunawa kwa mfumu.

14. Nebukadinezara anayankha, nati kwa iwo, Kodi mutero dala, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, kusatumikira milungu yanga, ndi kusalambira fano lagolidi ndinaliimikalo?

15. Mukabvomereza tsono, pakumva mau a lipenga, citoliro, zeze, sansi, cisakasa, ndi ngoli, ndi zoyimbitsa ziri zonse, kugwadira ndi kulambira fano ndinalipanga, cabwino; koma mukapanda kulambira, mudzaponyedwa nthawi yomweyi m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto; ndipo mulungu amene adzakulanditsani m'manja mwanga ndani?

16. Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu.

17. Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.

18. Koma akapanda kutero, dziwani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.

19. Pamenepo Nebukadinezara anadzazidwa ndi ukali, ndi maonekedwe a nkhope yace anasandulikira Sadrake, Mesake, ndi Abedinego; anayankha, nati asonkheze ng'anjo kasanu ndi kawiri koposa umo amasonkhezera.

20. Nauza amuna ena amphamvu a m'khamu lace la nkhondo amange Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ndi kuwaponya m'ng'anjo yotentha yamoto.

21. Pamenepo amuna awa anamangidwa ali cibvalire zopfunda zao, maraya ao, ndi nduwira zao, ndi zobvala zao zina; naponyedwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

22. Motero, popeza mau a mfumu anafulumiza, ndi ng'anjo inatentha koposa, lawi la moto linapha iwo aja ananyamula Sadrake, Mesake, ndi Abedinego.

23. Ndipo amuna atatu awa, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, anagwa pansi omangidwa m'kati mwa ng'anjo yotentha yamoto.

24. Pamenepo mfumu Nebukadinezara anadabwa, nauka msanga, nanena nati kwa mandoda ace, Kodi sitinaponya amuna atatu omangidwa m'kati mwa moto? Anayankha nati kwa mfumu, Inde mfumu.

25. Anayankha, nati, Taonani, ndirikuona amuna anai omasuka, alikuyenda m'kati mwa moto; ndipo alibe kuphwetekwa, ndi maonekedwe a wacinai akunga mwana wa milungu.

Werengani mutu wathunthu Danieli 3