Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 2:31-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Inu mfumu munapenya ndi kuona fano lalikuru. Fanoli linali lalikuru, ndi kunyezimira kwace kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ace anali oopsa,

32. Pano ili tsono, mutu wace unali wagolidi wabwino, cifuwa cace ndi manja ace zasiliva, mimba yace ndi cuuno cace zamkuwa,

33. miyendo yace yacitsulo, mapazi ace mwina citsulo mwina dongo.

34. Munali cipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ace okhala citsulo ndi dongo, nuwaphwanya.

35. Pamenepo citsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo ao; ndi mwala udagunda fanowo unasanduka phiri lalikuru, nudzaza dziko lonse lapansi.

36. Ili ndi loto; kumasulira kwace tsono tikufotokozerani mfumu.

37. Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wa Kumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikuru, ndi ulemu;

38. ndipo pali ponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakucititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolidi.

39. Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wocepa ndi wanu, ndi ufumu wina wacitatu wamkuwa wakucita ufumu pa dziko lonse lapansi.

40. Ndi ufumu wacinai udzakhala wolimba ngati citsulo, popeza citsulo ciphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga citsulo ciswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.

41. Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zace, mwina dongo la woumba, mwina citsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya citsulo; popeza mudaona citsulo cosanganizika ndi dongo.

42. Ndi zala za mapazi, mwina citsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo, mwina wolimba mwina wogamphuka.

43. Ndi umo mudaonera citsulo cosanganizika ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma sadzapharikizana, monga umo citsulo sicimasanganizikana ndi dongo.

44. Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzao nongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wace sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse nudzakhala cikhalire.

45. Umo mudaonera kuti mwala unasemedwa m'phiri popanda manja, ndi kuti udapera citsulo, mkuwa, dongo, siliva, ndi golidi; Mulungu wamkuru wadziwitsa mfumu cidzacitika m'tsogolomo; lotoli nloona, ndi kumasulira kwace kwakhazikika.

46. Pamenepo mfumu Nebukadinezara anagwa nkhope yace pansi, nalambira Danieli, nati amthirire nsembe yaufa ndi ya zonunkhira zokoma.

47. Mfumu inamyankha Danieli, niti, Zoona Mulungu wako ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa mafumu, ndi wobvumbulutsa zinsinsi; popeza wakhoza kubvumbulutsa cinsinsi ici.

Werengani mutu wathunthu Danieli 2