Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzao nongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wace sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse nudzakhala cikhalire.