Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 2:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka caciwiri ca Nebukadinezara mfumu, Nebukadinezarayo analota maloto, ndi mzimu wace unabvutika, ndi tulo tace tidamwazikira.

2. Pamenepo mfumu inauza munthu aitane alembi, ndi openduza, ndi aula, ndi Akasidi, amuululire mfumu maloto ace. Nalowa iwo, naimirira pamaso pa mfumu.

3. Niti nao mfumu, Ndalota loto, nubvutika mzimu wanga kudziwa lotolo.

4. Pamenepo Akasidi anati kwa mfumu m'Ciaramu, Mfumu, mukhale ndi moyo cikhalire: mufotokozere anyamata anu lotoli, ndipo tidzakuuzani kumasulira kwace.

5. Niyankha mfumu, niti kwa Akasidi, Candicokera cinthuci; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lace, mudzadulidwa nthuli nthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.

6. Koma mukandidziwitsa lotoli, ndi kumasulira kwace, mudzalandira kwa ine mphatso, ndi mphotho, ndi ulemu waukuru; cifukwa cace mundidziwitse lotoli ndi kumasulira kwace.

7. Nabwerezanso iwo kuyankha, nati, Mfumu ifotokozere anyamata ace lotoli, ndipo tidzaidziwitsa kumasulira kwace.

8. Mfumu inayankha, niti, Ndidziwatu kuti mukunkhuniza dala, pakuona inu kuti cinthuci candicokera.

9. Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; cifukwa cace mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwace komwe.

10. Akasidi anayankha pamaso pa mfumu, nati, Palibe munthu pa dziko lapansi wokhoza kuulula mlandu wa mfumu; cifukwa cace palibe mfumu, mkuru, kapena wolamulira, wafunsira cinthu cotere kwa mlembi, kapena wopenduza, kapena Akasidi ali onse.

Werengani mutu wathunthu Danieli 2