Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 11:8-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndi milungu yao yomwe, pamodzi ndi akalonga ao, ndi zipangizo zao zofunika za siliva ndi golidi adzazitenga kumka nazo ndende ku Aigupto; ndi zaka zace zidzaposa za mfumu ya kumpoto.

9. Ndipo adzalowa m'ufumu wa mfumu ya kumwela, koma adzabwera m'dziko lace lace.

10. Ndi ana ace adzacita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akuru ocuruka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzacita nkhondo mpaka linga lace.

11. Ndi mfumu ya kumwela adzawawidwa mtima, nadzaturuka kulimbana naye, ndiye mfumu ya kumpoto imene idzaonetsa unyinji waukuru; koma unyinjiwo udzaperekedwa m'dzanja lace.

12. Ndipo ataucotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wace; ndipo adzagwetsa zikwi makumi makumi, koma sadzalakika.

13. Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wa kuposa oyamba aja; nidzafika pa cimariziro ca nthawi, ca zaka, ndi khamu lalikuru la nkhondo ndi cuma cambiri.

14. Ndipo nthawi zija ambiri adzaukira mfumu ya kumwela, ndi aciwawa mwa anthu a mtundu wako adzadzikuza kukhazikitsa masomphenyawo, koma adzagwa iwo.

15. Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda midzi yamalinga; ndi ankhondo a kumwela sadzalimbika, ngakhale anthu ace osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.

16. Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzacita cifuniro cace ca iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pace; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwace mudzakhala cionongeko.

17. Ndipo adzalimbitsa nkhope yace, kudza ndi mphamvu ya ufumu wace wonse, ndi oongoka mtima pamodzi naye; ndipo adzacita cifuniro cace, nadzampatsa mwana wamkazi wa akazi kumuipitsa; koma mkaziyo sadzalimbika, kapena kubvomerezana naye.

18. Pambuyo pace adzatembenuzira nkhope yace kuzisumbu, nadzalanda zambiri; koma kalonga wina adzaleketsa kunyoza kwace adanyoza nako; inde adzambwezera yekha kunyoza kwace.

19. Pamenepo adzatembenuzira nkhope yace ku malinga a dziko lace lace; koma adzakhumudwa, nadzagwa osapezedwanso.

20. Ndipo m'malo mwace adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo; koma atatha masiku owerengeka adzatyoledwa iye, si mwamkwiyo, kapena kunkhondo ai.

21. Ndi m'malo mwace adzauka munthu woluluka, amene anthu sanampatsa ulemu wa ufumu, koma adzafika kacetecete, nadzalanda ufumu ndi mau osyasyalika.

22. Ndipo mwa mayendedwe ace a cigumula adzakokololedwa pamaso pace, nadzatyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa cipangano.

23. Ndipo atapangana naye adzacita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka.

Werengani mutu wathunthu Danieli 11