Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 11:28-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo adzabwerera ku dziko lace ndi cuma cambiri; ndi mtima wace udzatsutsana ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace, ndi kubwerera ku dziko lace.

29. Pa nthawi yoikika adzabwera, nadzalowa kumwela; koma sikudzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.

30. Pakuti zombo za ku Kitimu zidzafika kuyambana naye; cifukwa cace adzatenga nkhawa, nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi cipangano copatulika, nadzacita cifuniro cace; adzabweranso, nadzasamalira otaya cipangano copatulika.

31. Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lace; nadzacotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa conyansa copululutsaco.

32. Ndipo akucitira coipa cipanganoco iye adzawaipsa, ndi kuwasyasyalika; koma anthu akudziwa Mulungu wao adzalimbika mtima, nadzacita mwamphamvu.

33. Ndipo aphunzitsi a anthu adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi lawi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.

34. Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling'ono; koma ambiri adzaphatikizana nao ndi mau osyasyalika.

35. Nadzagwa aphunzitsi ena kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthawi ya citsiriziro; pakuti kukaliko kufikira nthawi yoikika.

36. Ndipo mfumu idzacita monga mwa cifuniro cace, nidzadzikweza, ndi kudzikuza koposa milungu iri yonse nidzanena zodabwiza pa Mulungu wa milungu, nidzapindula, mpaka udzacitidwa ukaliwo; pakuti cotsimikizika m'mtimaco cidzacitika.

37. Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ace, kapena coikhumba akazi, kapena kusamalira milungu iri yonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.

38. Koma kumalo kwace idzacitira ulemu mulungu wa malinga; ndi mulungu amene makolo ace sanaudziwa, adzaulemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wace, ndi zinthu zofunika.

39. Ndipo adzacita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wacilendo; ali yense wombvomereza adzamcurukitsira ulemu, nadzawacititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wace.

40. Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwela idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kabvumvulu, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.

41. Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lace ndi awa: Edomu, ndi Moabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

42. Adzatambalitsiranso dzanja lace kumaiko; dziko la Aigupto lomwe silidzapulumuka.

43. Ndipo adzacita mwamphamvu ndi cuma ca golidi, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Aigupto; Alubi ndi Akusi adzatsata mapazi ace.

Werengani mutu wathunthu Danieli 11